Ntchito yakukhosi kwanu njiti?

Umunthu uzigwilizana ndi ntchito yakukhosi kwanu. Yankhani mafunso awa kuti muwone ngati akulozela ntchito yakukhosi kwanu.

1. Mukamawonela kanema chidwi chanu chimakhala pazinthu ziti?

A) Kukongola kwa chilengedwe kapena nthumazi ya anthu amufilimu B) Ndeu (zomenyana), kuvuvuma kwa magalimoto kapena mmene filimu ikulilimila C) Ndalama zimene zalowa kuti apange filimu komanso kuti anthu alimmenemo alandila ndalama zingati

2. Pamene muli ndi amnzanu kocheza kaya pazochitika zapasukulu chimwemwe chanu chimawoneka chotani

A) Mumathamangila kutsogolera zinthu ngati KUYIMBA, magemu kapena kuthamangila pachakudya B) Inu ndi amene mumawonetsetsa kuti mwatenga mbali yoti anthu ayitanidwa pazochitika komanso abwere panthawi yake. C) Ine ndiye amene ndimatsogolera kafukufuku wina aliyense, kupeza malo amsonkhano, komanso kudziwa kuti tilipila ndalama zingati kwa eni malowo

3. Mukakhala ndi vuto mumapulumukila pati?

A) Ndimadziwa kalankhulidwe kake B) Manja anga amandichitila ubwino C) Ndimakonda kupanga kafukufuku, kuwerenga mabuku kusukulu mpaka ndipeze yankho

4.Tiyelekeze muli ndi munda kaya dimba lamasamba koma mbeu zagwidwa matenda mungatani

A) Nditha kuzikambila kankhani mbewuzo kapena kuyimba tinyimbo B) Ndingayesetse kupeza mankhwala achikuda C) Nditha kupondaponda komanso kugundika ndi kafukufuku mpaka ndipeze vuto lenileni ndisanapeze yankho

Pali phindu lina lililonse

Mgulu loyamba

Ukusonyeza kuti uli ndi chidwi komaso luso. Ndiiwe okonda kuthandiza anthu komanso umalingalira zinthu mozama. Anthu aluso amachita bwino pantchito maka kuimba, kulemba, utola nkhani, uphunzitsi, zamafasho ndi ntchito zotukula madela

Mgulu lachiwiri

Umakonda kuwunika zinthu kupanga kafukufuku kuti uwone chiyambi komanso gwero lake. Ntchito ya zascience, kufactory, ulimi, umakaniko kapena factory yazakudya ndiyoyenela iwe

Mgulu lomaliza

Ndiwe munthu wolakalaka kuti udziwe momwe ungachitile chinthu. Kaya kafukufuku. Ngati masamu ndikudya kwako ndiye kuti ntchito yowerengela ndalama singavute kapena business imene.

Ngati ndiwe wokonda kuwerenga ndiye kuti ungakwanitse kukhala lawyer, kugwira m'boma kapena sukulu yaukachenjede.

Share your feedback