Agogo, ndili ndi mzanga amene ali mayi wachisodzera ndipo amakonda kukhala okhumudwa. Kodi ndingamulimbikise bwanji?

Ineyo ndikudziwapo atsikana angapo omwe anabeleka akadali achichepele nawonso anadutsa muchipsinjo ngati mnzakoyu koma pano akusimba lokoma. Apatu sindikutanthauza atsikana okha ayi ngakhalenso anyamata amene amakhala kholo akadali achichepele.

Ambiri mwaiwo sanapulukile nazo ayi pano akusimba lokoma. Ndibwino kuti uli ndichidwi chofuna kuthandiza komanso ukufuna kumamulimbikitsa mnzakoyu. Apatu kwake ndikuyamika basi ngakhale kungavute kutero. Uziyesetsa kupanga zinthu zansangala komanso zokukomelani nonse kaya kuimba, imbani nyimbo zimenenso mnzakoyo amazikonda.Ngati mnzakoyu anabwelera kale kusukulu ndibwino kumamuthandiza zina ndi zina kuphatikiza homework.

Koma ngati maganizo oyambanso sukulu ali nawo kutali uthabe kumamamukambira nkhani zokhudza sukulu kuti nayenso akhale ndi chidwi. Zotelezi zingathe kuthandiza kulimbikitsa ubwezi wanu.

Share your feedback