Khalani Wokondeka Waokondedwa Wanu

Kuyambila lero mpaka muyaya

Palibe chimango china chingapose abwenzi omwe akondana kwambiri. Ngakhale abwezi achuluke chotani pamakhalabe ena mwaiwo otolelana nawo kwambiri.

Abwezi abwino ndiwomwe umawakhulupilira kwambiri amasunga chinsinsi chako ngakhale chingaopse chotani.

Pali abwezi palinso zochitika zambiri koma nkhani yayikulu ndikusamala chibale. Kuti musathe mtunda olo kuluza bwezi lako yeselani zinthu izi:

Pewani kupanga mpikisano

Aliyense ndi dolo payekha. Palibe chifukwa chochitilana nsanje ayi. Ngati mnzako akukuposa chinthu iweyo ulinso ndikuthekela kwina koposa iye. Nonse muli ndi luso lapadeladela.

Lankhulani mwachilungamo

Ena amati kupepesa ndikupepela koma sichonchoyi. Kulankhula chilungamo ndi mtima onse ndikovuta ndithu. Pena pake chilungamo chimawawa kulibwino kuvomela ndi mutu kapena chamumtima.

Mwachitsanzo ngati mnzanu wabeka mabisuit sibwino kuwonetselatu kunyasidwa kwanu. Sungani ulemu ponena kuti, ''Ndikutha kuwona utapindula ndi khama lako makamaka utatsata ina monga kubeka motsatila ndondomeko iyi, uwona zikhalanso bwino.'' Pakutelo mnzako sangawawidwe mtima chifukwa wanena mwaulemu.

Musasiye kuyamikila

Ndibwino kuyamikila ntchito yabwino yomwe mnzanu wachita. Apa sitikutanthauza kuti mukonde zithunzi zonse zamunthu pa facebook ayi. Aliyense amasangalala ngati wamva liwu lomuyamikila.

Njoyani limodziCelebrate together

Bwenzi labwino limasangalala mnzake akapambana. Ngati mnzako wakhoza nambala yabwino mkalasi muyamikile. Njoyani ndithu. Choona chenicheni nchakuti apa ndizachidziwikileni kuti anthuwa anali ndi cholinga maka analimbikila sukulu zatheka.

Kuthandizana komanso kugwila mnzako dzanja panthawi yamavuto

Share your feedback