Simutolelana ndi abwezi anu?

Zizindikilo zake nazi...

M'dziko muno muli anthu osiyanasiyana ndipo sungakhale bwezi laonse ayi. Njira yabwino kupala ubwezi ndiena ndikudziwa adani ako.

Mdani wako ndiyemwe amakusowetsa mtendele

Ngati ukusowa mtendere pamene uli ndi munhtu wina kapena munthuyo akufuna umpangile chinthu chomwe iwe sukusangalatsidwa nacho ndibwino kumutaya. Ayendele yake.

Amakunyogodola

Bwezi lako limakulemekeza. Ngati wina akutonza, kukunyogodola ameneyo siwocheza naye.

Samalabadila zonena zako

Anthu amatama komanso akhwidzi amakupepeletsa kukutenga iwe ngati kape iwo mabwana.

Nanji ukakhala ogona amakulowa mkati iwe osawothelanso. Koma akakutenga ngati bwezi lawo ndibwino kuti Pakhale chibale komanso alemekeze maganizo ako.

Umashela ukakhala pakati pawo

Abwezi abwino umasangalala nawo limodzi. Chenjera ndi anthu omwe amakonda kunena ndi kunyoza amnzawo mapeto ake adzakukopa kukhala mmodzi mwaiwo.

Kunena toto ndikovuta ngakhale pamaso pamdani wako komabe ndibwino. Ngati ukufuna kupita patsogolo ndi moyo khala pamabwalo a anthu okhawo akufuna kwabwino chifukwa iwo adzakulimbikitsa kuti maloto ako aphelezele.

Share your feedback