ZATHU IYANKHULA KWA OYIMBA OZITSATA MU AFRO POP PA ZA KULIMBA MTIMA

Nkhani Ya Janta....

Dzina langa ndi Shukuran Mwachumu, koma lodyela ndine Janta. Ndimaimba Nyimbo za Afro Pop. Ndine wamtundu wachiyao. Ndimachokela ku Zomba.

Makolo anga poyamba samandilimbikitsa zazoimbaimbazi ayi. Sizinali zophweka komabe ndinalimbikila kupusha ngakhale ndinali pakati pazipsinjo.

Chifukwa cholimbikila ndi kupilira kwanga panopa dzina langa pazoimbaimba lakhazikika ndilinso ndi fans yondikonda.

Makolo anga ndi achibale pano amasapota ntchito yangayi. Aliyense panopa amadziwa kuti Janta ali ndi chamba chake chotchuka MMalawi muno chomwe chili chophatikiza chikhalidwe chathu komanso chachichizungu.

Ndinakwanitsa kuika Malawi Pa Map ndikaimbidwe kangakanga. Anthu akamva maimbidwe anga kaya kavalidwe amadziwa kuti uyu ndi Janta. Anthu amatolapo nzeru komanso kupeza phindu mmayimbidwe anga mpaka kupezeka asintha khalidwe.

Ndipezelepo mwayi apapa ndilimbikitse atsikana. Ndimatamanda ma pulogaramu omwe akupititsa patsogolo komanso kupeleka mwayi kwa atsikana. Ngati mtsikana akufuna kuti aziimba ngati mmene ndikuchitila inemu sizikutanthauza kuti iyeyo wataika ayi ngati momwe anthu ena amaganizila. Nthawi yakwana yoti anthu alemekeze zokhumba atsikana pamene akutsatila maloto awo komanso zosangalatsa moyo wawo. Nyimbotu zagona pa uthenga ndipo atsikana ali ndi gawo lalikulu lomwe tingaligwiritse ntchito mu nyimbo.

Share your feedback