Kulimba Pakati Pamikwingwirima: Kuphunzira Kuchokera Kwa Memory Banda

Nkhani ya Memory Banda.....

Dzina langa ndine Memory Banda , ndipo ndimagwila ntchito ngati Project Coordinator.

Ndili wamg’ono, makolo anga sankasangalala ndi maganizo anga opitiliza maphunzilo. M’malo mwake, amafuna ndilowe m’banja, chifukwa choti anzanga ambili ali ndi ana komanso anakwatila kale. Komabe ine sindinalole kuti ndilowe m’banja ndisanamalize sukulu, choncho ndinalimbikilabe kupita kusukulu.

Lero, kumudzi amandilemekeza chifukwa choti ndinaphunzila ndipo amawauza ana ena kuti atengere chitsanzo changa. Zimene ndinasankhazi zinathandiza kuti makolo anga komanso abale anga asinthe m’mene amaonela zinthu.

Tsiku lina ndikufuna anthu adzandikumbukile kuti ndinathandiza kusintha chikhalidwe cha anthu. Pakadali pano ndimathandiza atsikana, achinyamata komanso makolo kuti asinthe maganizo awo okhudza momwe amaonela maphunzilo komanso kupititsa atsikana ku sukulu.

Mwina nanunso mukukumana ndi zomwe zinandichitikila ine. Malangizo anga kwa inu ndi otere; si kolakwika kuwaunikila makolo ngati akupanga chiganizo cholakwika, nthawi zina ndi bwino kuwafotokozera zomwe mukufuna mwa ulemu ndi kuwaunikila ubwino wa sukulu osati kukwatila uli wan’gono.

Share your feedback