Mphatso

Yemwe ndi Theresa

Mzimayi wachisodzela yemwe analekezela sukula panjira. Ali ndi ‘sugar daddy’, komabe akulakalaka atabwerelanso pasukulu ndi kukhala odziimila payekha. Mphatso akutipatsa phunziro lakuti tisamalekelele kale lathu kutibweza mmbuyo kapena kugwa mphwayi kukwanilitsa zokhumba zathu.

“Ndinafunsila ntchito ku Zathu chifukwa mnamvetsedwa kuti Zathu ikhala pulogaramu ya achinyamata yapamwamba muno M’malawi choncho ndinaganiza isandiphonye. Nduona kuti Zathu iyanjanitsa chimnzake pakati pa atsikana ndi anyamata; ipeleka mwayi kwa anyamata ndi atsikana wofunsa mafunso momasuka komanso mopanda kuweluzidwa.” Theresa

Share your feedback