BWANA MKUBWA WA MHUB AKAMBA ZA MOYO WAKE: NKHANI YOKHUZA MAPHUNZIRO MKATIKATI MWA MAVUTO

Nkhani Ya Vincent Kumwenda....

Dzina langa ndine Vincent Kumwenda, ndine wamkulu wa bungwe la Mhub. Zaka zingapo zapitazo nditamaliza secondary sukulu yanga ndinapeza mwayi wopitiliza maphunzilo ku University.

Tsoka ilo patangotha miyezi ingapo ndinalephela kupitiliza maphunzilo chifukwa chosowa fizi. Ndinalibe ndalama komanso thandizo lina lililonse mpaka ndinasiya sukulu.

Ndinayesayesa kuyang’anayang’ana njira zopezela ndalama ya fizi popanga timaganyu tina ndi tina mtawuni. Ngati njira imodzi yoti ndisathawane ndi amnzanga pamaphunzilo komanso kuti mwina ndiyese kupeza degree yanga ndimakawelenga ku library ku Blantyre. Ndinalimbikila kwambiri kuwerenga pandekha uku ndikutolera tindalama toti ndidzathe kulembela mayeso.

Ndimamisa zinthu zambiri zochitika pasukulu monga maulendo apasukulu wokaphunzila zinthu zina komanso zamasewerasewera. Sindimaloledwa kulowa mu library yapasukulu pakuti sindinalipile fizi.

Izi zinandisawutsa kwambiri chifukwa panalibe china chomwe ndimkafuna pamoyo wanga ngati mnyamata kuposa sukulu. Ngakhale ndimakumana ndi zokhoma chonchi ine sindinataye masomphenya anga ayi.

Chidwi changa chinali pa technology ngakhale pachiyambi changa ku college ndinasankha maphunzilo ena. Nditamaliza college ndinaganiza kuti ndisasiyile pompo ndipo ndinakalembetsanso sukulu ku Technobrain nkukayamba maphunziro otchedwa Information Technology.

Apatu panali posavuta kwa ine kupeza ntchito ku Mhub. Mhub ndi malo okhawo muno M’malawi omwe zochita zawo zagona pa luso la technology komanso ndi malo omwe timathandiza achinyamata luso lawo pa technology ndi mabizinezi/ntchito zamanja kuti akwanilitse maloto awo.

Maphunzilo andipititsa ine patsogolo komanso kutsekula mwayi wambiri pokweza ntchito yanga. Mwachitsanzo, panopa ndinasankhidwa kukhala mmodzi mwa achinyamata 19 amene tikhale tikupita ku dziko la Amerca mwezi wa June kukatenga nawo mbali mu pulogaramu ya Young African Leaders Initiative, YALI.

Komansotu masiku akubwelawa, posachedwapa ndikhala ndikupita ku dziko la China kumene kuli maphunzilo otukula achinyamata kwa masabata atatu.

Kwa anyamata amnzanga omwe akusawutsika ndi fizi ndi mavuto ena limbikitsidwani kupeza njira zothana ndi mavuto anu. Musasiye sukulu, limbikani kuti maloto anu aphelezele. Khama lipindula.

Share your feedback