KUGONJETSA CHIKHALIDWE CHOTCHINJILIZA ATSIKANA: NKHANI YA MZIMAYI OYIMBILA MPIRA WAMIYENDO

Nkhani ya Martha Nyekenka...

Ndine Martha Nyekenka. Ndakhala ndikuimbila masewera a mpira kuyambila mchaka cha 1999 koma pano ndinapuma (ndinapanga retire). Mbiri yanga ili motere.

Ine ndili mtsikana wang’ono ndakulila limodzi ndi anyamata omwe ndimakonda kusewera nawo mpira wamiyendo.

Chidwi changa pampira chinayamba ndili wang’ono kwambili ngakhale vuto linali loti panthawiyi kunalibe mpira wamiyendo waatsikana M’malawi muno. Sichinali chinthu chapafupi kupeza mtsikana akusewera mpira wamiyendo, palibe amalolezedwa olo pang’ono.

Mchaka cha 1998 ndinayamba ntchito ku Malawi National Council of Sports ndipo mchaka chomwecho bungwe la PSI linakhazikitsa mpira wamiyendo waatsikana. Ine chidwi chosewela mpira chinachoka ndinayamba kuimbila. Zitatelo ndinayamba ntchitoyi ngati Administrator. Ndinasankhidwa kukhala mlembi woyamba mu Blantyre Women’s league. Ndipo ndikugwirabe za administration ndinalembetsa maphunzilo a zoimbila mpira, yotchedwa ‘Referee Training and Sports administration.’ Mchaka cha 1999 ndinasiya ntchito ndikuyamba za u-referee ngati ntchito yanga yokhazikika.

Mu 2003 ndinayamba kuimbila mpira mu super league, imene ili league yaikulu ya mpira wamiyendo muno M’malawi komanso ndimaimbila magemu ena akunja.

Chifukwa chakukhazikika zaka zingapo pantchitoyi ndinapatsidwa certificate ya FIFA ngati mphunzitsi kapena kuti Instructor. Pakali pano ndimaphunzitsa muno M’malawi komanso nthawi zina Afifa amanditenga kukawaphunzitsila anthu ena.

Ndimakumbukila mpira wamiyendo waatsikana utayamba kumene makolo anga anali ndi mantha kuti mwina nditha kupweteka ndili mkati moponya mpira olo kutenga mbali ina iliyonse.

Ndimakumbukila ndikuwauza kuti ayi sindikuponya nawo ndikungoimbila chabe. Mayi anga anandilimbikitsa komanso kuvomeleza kuti ineyo chidwi changa chili pampira basi ngati momwe aliri amnzanga ena achinyamata omwe ndakula nawo.

Ndakumana ndisopinga zambiri pantchito imeneyi. China mwaizo nchakuti oimbila amnzanga aamuna amakana kuimbila gemu limodzi ndi oimbila aakazi. Ambiri mwaiwo amati anthu akazi sangakwanitse kuimbila mpira wamiyendo womwe amuna amanga nthenje.

Ndimakumbukila nthawi ina kunali mpikisano wa Coca Cola womwe oimbila ena anali akunja. Ine ndinali oimbila yekhayo wamkazi pa panel. Amnzanga ena apa panel anasangalala nane makamaka oimbila wochokela ku Zambia. Iyeyu ananena poyela kuti anali munthu mmodzi wonyozela kuti akazi angakwanitsa kugwira ntchito zomwe amuna amagwira m’masewera amene amuna anamanga nthenje.

Share your feedback