Njira zosungila ndalama ndi bwezi lako

Kusunga ndalama ndikokoma … kumabweletsa phindu lalikulu

Mmbuyomu takhala tikukambilana zatsogolo lathu ine ndi Habiba. Habiba akufuna atakhala mphunzitsi. Ine koma namwino. Vuto tili nalo ndi nkhani ya makobidi. Masiku ano maphunziro ndi mnthumba. Choncho tinaganiza zoyamba kuseva ndalama. Pano tili ndi mpamba ndithu mutha kudabwa koma izi zatheka chifukwa:

Timamvana. Tilibe dzibwana

Tinamanga nfundo yoseva ndalama limodzi chifukwa timakhulupilirana kwambili. Pachiyambi, tinakambilana za cholinga chathu ndikuchilemba mmakope tisayiwale. Nthawi zonse ndalama yotuluka timalemba mmakope osayiwala tsiku lake(Date). Pakatha sabata ziwiri timatsatila mmakope kuwona mmene zikuyendela kupewa kukayikilana.

Timathandizana komanso kuchenjezana

Pamene tili pagulu la amnzathu ndipo ena akugula zopanda pake ife timachenjezana. Ndikakhala pandekha opanda Habiba ndimayenela kumudziwitsa kaye ndisanawononge ndalama.

Kutsinana khutu musanawononge ndalama

Mwezi uli wonse timakhala pansi ndikuwona zolinga zamwezi umenewo. Kodi tiseva ndalama zingati? Tikatelo basi kuwusumana mwina Kandalama kotsalako tilaweko ka-Cake.

Timalimbikitsana

Ndikadziwa kuti cholinga changa chindigwetsa ndimathawila kwa Habiba kuti andiwunikile. Kuseva ndalama ndi mnzako zimathandiza. Zikakukoka manja umatsamila pamnzako komanso ukasokela mnzako amakukonza.

Timathandizana

Masiku apitawa Habiba anapita kuchikwati koma chosangalatsa nchakuti mmalo moti avale malaya anyuwani sanadzilowe nthumba. Mwachidule anangopempha kuti ndimubweleke malaya anga. Pamane tikuvalilana zovala kaya kudyela lunch pamodzi zikuthandiza kuti thumba lathu likule.

Share your feedback