Dzina langa ndine Moses ndimachokela ku Mzimba. Gogo, ndakhala ndikuyesela zambiri kuti mwina ndibooleze luso langa. Koma nthawi zina ndimaona ngati ndili ndi luso lojambula makatuni ngakhale pena amnzanga amaseka zojambula zanga. Kodi ndingatani?
Mwana wanga, aliyense ali ndi luso lake-lake. Ena anabadwa nalo pamene ena amachita kuphunzilira kapena kungokhala akhama ndi kugwiragwira.
Inetu ndiwosangalala kuti iweyo wazindikila chomwe umatha ndipo ngati umasangalatsidwa nacho ine ndikulimbikitse kuti pitiliza chifukwa ndi njira yokhayo yopititsa mtsogolo luso lako. Ichitu chimakhalanso chinthu chothandiza anthu kulankhula zakukhosi kwawo.
Komansotu zindikila kuti palibenso chifukwa chakuti utanganidwe ndikusakasaka kuti luso lako lagona pati.
Mwayi Kumwenda, amasewela mpira wa mnchembere mbaya kapena Gabadhino Mhango, woponya mpira waanyamata wamiyendo ndi zitsanzo zabwino za anthu omwe anachita bwino chifukwa choyika chidwi pa maluso awo.
Share your feedback