Moni gogo. Kodi ndikotheka kukwanitsa zokhumba zanga pamene ndatha nsinkhu nanga sindie kuti pamenepa sindinenso mwana?

Umu ndi momwe Gogo analiyankhila funsoli

Kutha nsinkhu sichachilendo mmoyowu pamene thupi lako likusintha. Pa chikhalidwe chathu pamakhala ziyembekezo zambiri pa atsikana kutino udindo wawo wasintha, chimodzimodzinso momwe zikhalira ndi mkazi wokwatiwa kapena mzimayi amene.

Kaya ndi maloto otani komanso zokhumba zomwe unali kuzilakalaka utha kuzikwanilitsa ngakhale kuti tsopano ndiwe mtsikana wachikulire, inetu ndingokulimbikitsa kuti usamamangike ayi pofuna kulankhula.

Upeze mnzako kapena wachikulire yemwe umamukhulupilira monga ngati aphunzitsi ako kuti akuthandize kukwanilitsa zolinga zako. Ndikuwona kuti uli ndi nkhawa kwambiri koma zindikila kuti palibe yemwe angakulepheletse kukwanilitsa maloto ako zingavute maka.

Share your feedback