Ndimakonda zojambula zithunzi kapena ndinene kuti ufotogalafa koma m’banja mwathu palibe alinane chidwi. Ndingawauze motani makolo anga kuti ndimanjoya ndikamagwira ntchitoyi?

Tsokalake achinyamata sikawirikawiri kulimbikitsidwa ma luso koma amati tiyike mtima pa sukulu basi. Langizo langa ndilakuti ngati nkotheka ukhale pansi ndimakolo ako uwafotokozele kuti umakonda kujambula zithunzi, ndipo zimakusangalatsa kwambiri, muli phindu komanso ntchitoyi nditsogolo lako.

Anthu ndife osiyana. Nthawi zina tikungoyenela kuwafotokozela anthu ena kuti atimvetsetse zofuna zathu.

Share your feedback