Kodi agogo, mtsikana atha kugwiritsa ntchito njira yakulera yapa ngozi?

Ana amnzanga, poyamba ndifotokoze kuti sitonse amene tikudziwa zamankhwalawa. Amenewa ndimankhwala apangozi oteteza mimba pamene mwina mwagonana mosadziteteza kapena njira yakulera yakanika.

Mwachitsanzo, nkutheka kuti mwagonana ndimwamuna ndipo mwangozi condom yaphulika. Mankhwala apangoziwa sakuyenela kugwiritsidwa ntchito ngati njira yakulera pokhapokha mwangozi basi. Ngati mwamwa mankhwalawa nthawi yangozi yomweyo kugwira ntchito kwake kumakhala kwa mphamvu kusiyana pakapita kanthawi.

Ngati mwamwa mochedwa nkutheka kuti mwatenga kale mimba pakuti mbeu ya bambo ikhoza kukhala kuti yakumana kale ndi dzila la mayi. Apa ndiye kuti mwayima basi. Mankhwalawa siwochotsela mimba ayi. Koma funso lako linali lakuti kodi mtsikana angagwiritse bwanji ntchito makhwalawa? Mankhwalawa amagulitsidwa kumafamase kapenanso kupelekedwa kuchipatala komanso Health Center.

Alipo mankhwala osiyanasiyana komabe akakufotokozelani bwino azachipatalawo. Muthaso kufunsa magwiritsidwa ake ngati simukudziwa. Koma chonde titsate ndondomeko yake. Kumbukani kuti kumwa mankhwala apangoziwa ndizothandidza kuteteza mimba zosakonzekela. Musamwe ngati njira ina yoteteza kutenga mimba ayi komanso mankhwalawa sateteza matenda opatsilana pogonana.

Share your feedback