Okondeka Agogo, nthupi mwangamu ndikumva ngati ndatha nsinkhu. Mabere anga atayamba kukula ndi zina, kwathu abale anayamba kumandisala. Kodi ndingatani?

Zikomo kwambiri funso limeneli atsikana ambiri limawasowetsa mtendere. Wanena zoona. Atsikana ena amachita manyazi akatha nsinkhu chifukwa matupi awo amayamba kusintha. Ngakhale enanso mwaiwo amanyadila ndikusinthaku.

Unamwali ndimbali imodzi yamoyo. Ndichizindikilo chakuti siiwenso mwana, koma wayambano ulendo wokhala munthu wamkulu. Mtsikana wachisodzela amachita nazo manyazi koma ndimomwe moyo ulili.

Chinanso ndichakuti makolo, amphwako ndi maneba atha kutenga mnamwali ngati mwanabe basi pamene iye mwini akudziwona kuti wakula. Choncho akhoza kumaona ngati chilichonse chonena iye kumachiwona ngati chachibwana izi zimakhumudwitsa.

Dziwani kuti pamene nsinkhu ukusintha thupi nalonso limasintha kaya maganizo komanso ziwalo pamenepa mpamene pamafunika wachikulire akhale nawe pansi kukubenthulira zina ndi zina.

Pamene uli ndi uthenga onse wokhudza unamwali maka kutha nsinkhu komanso ukukhala pakati pa anthu odalilika manyazi onse azomwe ukukumana nazo amatha.

Share your feedback