Nzovuta kukhala ndi ndalama zako pomweponso kupeza ntchito yapamtima pako. Ngati sungakwanitse kukafuna ntchito kulibwino kugwiritsa ntchito luso lbadwa nalo nkumapha makwacha
Mwayi wa Chikondi
Ndiwe namatetule pazophikaphika? Amnzanu akadziwa kuti amene ali kukhitchini ndi iwe tsiku limenelo amatekeseka nawe ndiangati? Yambani kugulitsa zophikaphika kaya totolatola ku sukulu.
Chikondi ali ndi zaka 13 ndipo wakhala akuthandiza mayi ake kuphika ali kamwana ndithu. ''Ndikakhala mmaluzi ndimaBeka makeke nkukagulitsa kwaamnzanga kusukulu. Ndimagulitsa pamtengo wozizila kuposa shop ina yapafupi ndi sukulu komabe anga amakhala a lero lomwe. Anthu amakonda afresh.''
Tawachi aphunzitsa munthu wina zasukulu
Tawachi ali ndi zaka 16 komatu akuchita zinthu zotamandika kwambiri. Iyeyu pamsikhu wakewu ndi mtichi kale. Pali ana atatu omwe akuwaphunzitsa akaweluka kusukulu kawiri pasabata. Tawachi akuti, ''mukamagawana zomwe mukuphunzila mudzapindula. Ine ndimapeza ndalama pothandiza anthu ena zasukulu.’’
Jermone ndi Luso lake
Jermone ali ndi zaka 18 koma atangokwanitsa zaka 15 anawonetselatu kuti ndipatali pankhani yojambula. Amapanga ma logo komanso maposter.'' Anthu ena amaphweketsa lusoli nkumati bola ntchito zolemetsa'' Chodabwitsa nchoti akawona zojambula kaya Malembo osiyanasiyana pa mashop samadabwa kuti zinabwela mndani, kapena ndi matsenga? Timachitatu kujambula ndi manja.
Jermone anayamba ndikujambula kenako kupanga makadi a anti ake amene business yawo ndi yomanga tsitsi. Apa anti ake anawuza amnzawo ena awiri.. Posakhalitsa Jermone anayamba kupeza makasitomala ambiri. Pakali pano iyeyu wayamba sukulu ya zojambulajambula ku college.
Share your feedback