Atsikana angathe!

Tiyeni timve zochitisa chidwi kuchokela kwa atsikana ena asanu zomwe zinachitila dziko ubwino

Masiku ano pali atsikana ambiri omwe achita zinthu zotamandika anthu osamvetsa. Apatu tili ndi atsikana asanu omwe dziko lagoma nawo .

Laura Dekker waku Netherlands ndi mtsikana yekhayo wachichepele yemwe anapalasa bwato kuzungulira dziko lonse payekha. Iye anapeza chilolezo kuBoma ndi kugonjetsa azamalamulo mpaka zinatheka. Laura anakwanitsa kuzungulira dziko lonse munzaka ziwiri ali ndi zaka 16.

Mikaila Ulmer anatsekula business yake ali ndi zaka 4 yotchedwa Me & the Bees Lemonade. Ichi ndichakumwa chosaledzeletsa. Mtsikanayu kangapo konse wanjitulidwako ndi njuchi chifukwa chakhama lake kuti awonetsetse kufunika kwa njuchi ngati mbali imodzi yazachilengedwe. Mapeto ake botolo lina lililonse logudwa amapatulako ndalama ina yoti ikatetezele njuchi.

Eva Tolage analemba kalata kwa Barak Obama, mtsogoleri wa America ali ndi zaka 14. Munkalatamu anamemeza mtsogoleriyu kuti achitepo kanthu pa umphawi omwe ulipo ku dziko lake la Tanzania komanso pa dziko lonse. Iye anawonjezeranso kunena kuti njala komanso maphunzilo kuphatikiza vuto la madzi ndi magetsi ndi zomwe zimawasowetsa mtendere iye ndi atsikana amnzake.. kalatayi inatakasa mitima yaazitsogoleri pamsonkhano wa United Nations ndipo anatengapo mbali.

Niloofar Rahmani ndi mtsikana woyamba yekhayo wachisilikali kuwulutsa ndege mmudziko la Afganistan. Ali mkati mwamaphunziro anatonzedwa kwambili pamodzi ndi makolo ake mu 2015. chifukwa chakulimba mtima kweke analandila mendulo kuchokela ku International Women of Courage Award.

Judi Lerumbe wochokela ku Kenya wazaka 15 ndimtsikana yekhayo yemwe anakwanitsa kugalukila abambo wake amene anamukakamiza kukwatiwa ndi chimdyamakanda. Mayi ake omupeza sanachitile mwina koma kugwirizana ndi Judi mpaka anathawila kumudzi wina kumene atsikana okhaokha ali pasukulu mmalo mwakwatiwa anakali achichepele.

Share your feedback