Moni Gogo. Dzina langa ndi martha ndimafuna ndidziwe ngati ndikoyenela kumalankhulana ndi anyamata pamene ndili kumwezi

Ndakhala ndikulandila mafunso ambiri angati funso loteleli ndie zikomo kwambiri polumikizana nane.

Poyamba, ndikofunika kunenelatu kuti chilungamo chake nchakuti palibe chomwe chingakuwonekele pamene ukulankhulana chabe ndi mnyamata pomwe uli kumwezi. Komansotu sikuti pamene uli kumwezi munthu aliyense adzichita kudziwa ayi pokhapokha iweyo wachita kusankha kuwuza anthu ena.

Komanso ndikofunikila kuti tilingalire zifukwa zomwe anthu anakuwuzila izi. Apatu ndikulimbikitse kuti ulankhule ndi yemwe anakuuza izi kuti umvetsetse maganizo awo komanso iweyo uthe kukhala ndi mwayi wokamba zakumtima kwako.

Share your feedback