T-Reel

Yemwe ndi Praise

Mnyamata wakhama, wolimbika ndipo sasunthika akamanga nfundo. Iyeyu amadzikhulupilira ngakhale kuti ndiokhumudwa ndi bambo ake omwe anachoka panyumba kalekale.

Nkhani ya T-Reel imadolola anthu ena mtima kuti naonso atsatile maloto awo mpaka zinthu kuyamba kuyenda.

“Nthawi zambiri chidwi chimakhala pa atsikana okha basi, anyamata amafila kuti mwawataya. Mtundu wathu wabweretsa mpikisano pakati pa anyamata ndi atsikana, koma Zathu yawonetsetsa kuti palibe atsale m’mbuyo koma atsikana ndi anyamata azisapotana wina ndi mnzake. Izi zithandiza kwa nthawi yoyamba kuti anyamata ndi atsikana agwire ntchito limodzi kuti zokhumba zawo zikwanilitsidwe.” Praise

Share your feedback