Timakhulupilira kuti ukapeza ntchito ya malipilo apamwamba moyo wathu udzasangalala. Koma ndalama sizigula chimwemwe.
Ngati mtima wako onse wagona pachomwe ukuchita mmoyo wako mdziko muno mwinanso nthawi yomweyo chinthuchi chikubweletsa ndalama ndiye kuti Chimwemwe chako chisefuka.
Mlembi wina waku Nigeria dzina lake Chimamanda Ngozi Adichie ali mwana aliyense amkayembekezela kuti adzakhala dokotala. Mwakuti iyeyu mpakana anakalowa mkalasi yazamankhwala.Chidwi cha Chimamanda chinali pamabuku. Kuyambila kuubwana wake anali ndi chilakolako cholemba.
Mwamwayi anapeza scholarship ndipo anapita ku America kukaphunzila luso lazolembalemba. Chaka chake chomaliza pasukulu buku lake linawina photho yayikulu zedi. Ambiri mwaife tikanawona ngati wataya nthawi bola akadapanga za udotolo koma iye anatsatila khumbo lake.
Kodi mumakonda kuphika kapena kuBeka? Muli ndi luso lina lapadela? Nanga achibale ndi amnzanu ena amakupemphani kuti muwathandize kusova masamu poti mumadziwa masamuwo? Nkhani ndiyakuti kuli bwino kunyindilira kuti ntchito yanu itsamile pamene pagona nzeru zanu.Nthawi zonse sizilira kukhala chimpamba kuti muyambepo. Kuthamanga sikufika. Mbewu ngakhale imodzi imabala mpaka kudzadza thumba. Mutha kuyamba kabusiness panyumba pogwiritsa achibale ndi amnzanu ena basi.
Khalani ndi tcheru kaya kusukulu. Ngati pali anthu ena amene ali kale pantchito yomwe mumayilakalaka funsani upangiri. Chitani kafukufuku mupeze njira yomwe mungatenge kuti muphule kanthu ndimaphunziro anu. Ngati sukulu yakulakani kapena mulibe pepala lililonse osada Nkhawa mungapindule ndi luso lanu. Koma dziwani ngati mukuchita bwino kusukulu makoma adzatsekuka mtsogolo.
Aliyense amafuna kupeza chochita pamoyo wake ndikukhala osangalala. Ndalama ili yachabe ngati tsiku ndi tsiku chidwi chogwila ntchito chathawa. Kukomela kwake nthawi ilipo yambili inu ndi achinyamata sinkhanisinkhani khumbo lanu.
Ngati simukukhutitsidwa tengani nthawi yanu muganizile mofatsa. Gwiritsani nthawi iyi polingalira zina pamoyo wanu.
Share your feedback