Zofunika kutsata komanso kupewa kuti ziphupu zithe

Ukhondo pathupi lathu (lisalale)

Chinyamata ndi nthawi yamtengo wapatali makamaka masinthidwe a thupi. Nkhope nayonso imasintha. Uwona yadzala ndi zibalobalo ngati siyinali yosalala konse.

Iyi ndinkhani yokhumudwitsa koma chosangalatsa nchakuti thandizo lake lilipo.

Nthawi yachisodzelayi, anyamata ndi atsikana matupi awo amasintha posakhalitsa ziphuphu kuyamba. Chiyambi chake ndichakuti nthawi imeneyi thupi limadzadza ndi poyizoni amene amatseka maglands opangila mafuta athupi.

Komabe iyi ndinyengo yakukula tisadele Nkhawa kapena manyazi ayi.

Zofunika kutsata komanso kupewa kuti ziphupu zithe:

Tisaphulitse

Tisaphulitse ziphuphu kuwopa majelemusi komanso kutupa pankhope. Kufiila komanso chipsela. Ngati mukuwona kuti mwatayika amnzanu akusalani ndibwino kuphitsa madzi amoto, fundani tawulo bafa kumaso ndipo nthuzi ija ikuwombeni kumaso pakutelo mabowo aja atsekuka ndipo chiphuphu chija chichoka mutu ndikupola.

Khalani aukhondo

Sambani kumaso mmawa ndi usiku uliwonse ndimadzi otentha komanso kasopo pang’ono. Musanyuleyi kapena kukhadabula thupi lanu. Kenako fundani bafatawulo yonyowa ndi nthuzi ija. Yesani mafuta ansatsi amafewetsa thupi.

Musakande

Musayelekeze kukanda/ kugwiragwira kumaso ayi kuwopa kuti majelemusi afikila nkhope yanu. Sambani mmanja nthawi zonse mukafuna kudzola mafuta kumaso.

Imwani madzi

Ndi madzi okha aukhondo omwe angatithandize kutsuka mapoyizoni nthupimu kuti tisalale. Kuwonjezela apo, madzi akumwa apatsa thupi lathu chitetezo chokwanila. Imwani madzi mmawa uliwonse ndipo tengani botolo la madzi kulikonse mupita.

Share your feedback