Ndikufunitsitsa nditapitiliza sukulu koma makolo anga akundikakamiza kuti ndiyike chidwi pa ntchito ya kumunda. Pamenepa ndingatani?

Umu ndi momwe Gogo analiyankhila funsoli…

Inetu ndakulira muno Mmalawi ndipo ndimadziwa kuti makolo ambiri amakonda kuphunzitsa ana kugwira ntchito molimbika powawuza kuti azigwira ntchito zapakhomo kapena tintchito tina ndi tina kumunda, palibe cholakwika ndi zotelezi, ndi chinthu chabwino kumatakataka pakhomo. Sindikudziwa kuti zili bwanji kwanuko komano kugwira ntchito kumunda sikutanthauza kuti basi sukulunso iyime ayi.

Nthawi zina tsoka limabwela chifukwa timayiwala kuti achinyamata amafunika nthawi yawo yachisodzela kuti atulukile chomwe ali popita kusukulu komanso kupanga masewera ndi zochitika zosangalatsa zina.

Koma nthawi zambiri achinyamata sapatsidwa nthawi yoti athe kuzindikila chomwe ali mmalo mwake amayembekezeledwa kuti azithandiza ntchito zapakhomo.

Ndizosangalatsa kuti makono zinthu zayamba kusintha pang’onopang’ono ndipo ndili ndi chiyembekezo kuti muzaka zikubwelazi makolo adzidzawamvetsetsa achinyamatawa.

Komano, kumbali yako iwe Madalitso zingakuchitile ubwino ngati utalankhulana ndi makolo akowo, kuwauza za khumbo lako lofuna kukhala pasukulu. Uthanu kumathandizila ntchito zapakhomo ukamaliza kuwelenga zakusukulu. Ngati mwina umachita manyazi utha kufunsa m’bale wako, aphunzitsi ako kapena wachikulire aliyense kaya ndi membala wa gulu la Amayi athe kulankhula nawo makolo ako mmalo mwako.

Share your feedback