Mungalimbe bwanji mtima komanso kukhala wamphamvu

Yeselani izi kuti mukhale olimba mtima

Kodi muli munyengo yamasautso ndipo mukusowa chochita? Sukulu siyikuyenda kuti mufunse nzeru mukulephela. Bwana wanu amakusowetsani mtendere koma simungayelekeze kusiya ntchito. Mukulakalaka mutayamba business koma kusowa nzeru. Mukufuna banja koma palibe chothamangila.

Ngati mukuwona mwathedwa nzeru kaya mwafooka kusowa chochita... ganizaninso kachiwiri.Zochita za Alesi ndizimodzi... amangoti... nzosatheka. Kwaiwo chilichonse ndichosatheka basi.

Mutha kukumana ndi masautso akulu mwina ndi anthu amene akukusawutsani kapena mukudutsa mnyengo yovuta kuti muchite ichi kulepheleka. Apatu sinthawi yogwa ulesi kuti gemu yagona.

Tikati nzosatheka tikutanthauza kuti:

• Sindikufuna • Sindikudziwa (ndithandizeni) • Sindingakwanitse

Pokhapokha mutakwanitsa kupewa kunena kuti nzosatheka ndipomwe mudzathe kupeza chadzetsa vuto chomwe nthawi zambiri chimakhala ulesi

Mmalo monena kuti sindikwanitsa kulibwino kunena kuti nditani ndipo mudzawonano kuti mmalo mwake mwakanilitsa izi:

• Ngati sukufuna palibenso kuchitila mwina chifukwa wanenelatu • Ngati mukusinkhasinkha kuti mungatani ndibwino kupempha thandizo kwawina. Pali mavuto ena oti akuthetsa nzeru, sungakwanitse, pezani munthu wokhulupilika ndikumubenthulira kuti mupepukidweko. Mukatelo ndiye kuti mwayamba bwino.

Chomaliza pazomwe tanenazi ndichakuti ngati mwataya chikhulupiliro kuti simungakwanitse chilichonse chidule chake ndikungosintha. Kulimba mtima simasewera ayi umayamba kugena kuchokela pazazing'ono. Chotsani chisimo chonena nzosatheka kuyambila lero. Konzekani kukhala ndi zolinga. Tengani mbali ina ya moyo. Maloto anu adzaphelezela.

Share your feedback