Gogo, nchifukwa chani zimawoneka ngati ndi nkhani yaikulu kuti mtsikana amalize maphunziro ake?

Kwa nthawi yayitali maphunziro a atsikana amawoneka osafunika komanso osalabadilidwa osati Mmalawi mokha muno komanso mmayiko ena.

Nthawi zina anthu amawona kuti maphunziro aatsikana asamawawerengere chifukwa chakuti amuna awo ndi omwe adzawasunge. Amaganiza kuti ntchito ya mai ndikusamalira pakhomo. Izi sizingachitile ubwino atsikana. Choncho anthu akhala akulimbana kuti zimenezi zisinthe.

Makolo pothandizana ndi ama bungwe akuyesetsa kutenga mbali kuthandiza atsikana kupita kusukulu ndikukhala ndi mwayi wangati wa anyamata. .

Kumbukilani mu sewero la Zathu, ndimamuchemelera Mphatso ndi Annetti amene anatha kubweleranso kusukulu komanso azinzawo a bandi amawathandiza.

Kumbukilani mu sewero la Zathu, ndimamuchemelera Mphatso ndi Annetti amene anatha kubweleranso kusukulu komanso azinzawo a bandi amawathandiza.

Share your feedback