Agogo, amnzanga amati mtsikana akakwanitsa zaka 23 ndipo sanagonaneko ndi mwamuna sadzabelekanso, ndizoona kodi?

Kayitesi, ili ndi bodza. Palibe mulingo uli wonse pazaka zoletsela kutenga mimba ngati mtsikana sanagonanepo ndi mwamuna. Izi zimachitika ngati munthu wasiya kusamba pamoyo wake.

Makamaka pamene mzimayi wafika zaka 45 kapena 50. Munthawiyi umasiya kupita kumwezi ndipo sungakhalenso ndi mwana ngakhale unabelekapo. Ngakhale unagonanapo ndi mwamuna kapena ayi. Umu ndimmene ziwalo za akazi zigwirira ntchito. Kusabeleka kutha kukhala ndi zifukwa zake zina koma osati chifukwa munthu wakhala nthawi osagonana ndi mwamuna ayi.

Share your feedback