Okondeka agogo, kodi ndibwino kulola achinyamata amene sali pasukulu kujowina gulu loyimba la band?

Zikomo kwambiri. Luso monga kuimba komanso ndakatulo ndinjira yothandiza anthu kulankhula zakukhosi kwawo. Luso loteleri limathandiza pamaphunziro.

Ngati pali mwayi obweleranso kusukulu zidalira iweyo kusula luso lako panthawi yoti ukungokhala kupititsa nthawi.Suwunanenepo chifukwa chomwe suuli pasukulu kapena ndi makobidi ngati momwe alili Annetti mu sewero la Zathu. Ngati ndichoncho ndietu uzitha kugwiritsa ntchito luso lakolo ndikumapeza kangachepe koti uthanso kumadzilipilira sukulu wekha.

Moyo penatu ndiosawutsa komabe muli ndikuthekela konse mutha kuchita bwino. Zabwino zonse.

Share your feedback