Okondeka agogo, ndizotheka kuti mtsikana amene watha nsinkhu ndizaka 12 kutenga mimba?

Zikomo kwambiri chifukwa cha funso lako. Nzoona kuti mtsikana wazaka 12 ndiwang’ono. Ngati watha nsinkhu ndipo akupita kumwezi ameneyu akagonana ndimwamuna mosadziteteza atha kutenga mimba.

Koma mtsikana wang’ono chonchi kutenga mimba ali pachiopsezo. Ziwalo zake ndizosakhwima makamaka njira zobadwitsila mwana. Apatu ndinthawi yoti mtsikanayu wayamba kukula. Ngati watenga mimba kawonaneni ndi Dokotala.

Mukuyenela kusamala chifukwa kupanda kutelo atha kuluza moyo. Adzakumana ndi mavuto ambiri pobeleka. Kutanga mimba unakali wang’ono sibwino ayi. Zotsatila zake ndizoopsa. Ndibwino kukhala ndi uthenga wokwanila wodzitetezela kumimba zotelezi. Funsani kwawachikulire akuthandizeni.

Share your feedback