Ana anga, pakatipa ndakhala ndikulandila mafunso kwa inu wokhudza ubwezi wogonana. Lero ndufuna ndigawane nanu mwazina zomwe mungazitsatile ngati inu ndi bwezi lanu mwasankha kuyamba kugonana.
Chinthu chofunikila kwambiri chomwe mukuyenela kudziwa ndi chakuti chisankho chogonana chiyenela kuti chichitike pogwirizana pakati pa inu ndi bwenzi lanu . Musadodome pofuna kukambilana zogonana ndi bwezi lanu musanagonane, komanso pezani langizo limodzi kapena panokha kuti mukhale odziteteza pa ubwezi wanu.
Ngati mwasankha kuti mufuna kuyamba kugonana wonetsetsani kuti mukugonana modziteteza pogwiritsa ntchito makondomu nthawi zonse. Izi sizikutetezani inu kumimba zosaziyembekezela kokha ayi komanso zikutetezani inu ku matenda osiyanasiyana opatsilana pogonana. Ndibwino kudziwa mmene mnthupi mwanu mulili pankhani ya HIV. Kuyezetsa magazi kumachitika ku mzipatala zonse ndi aphungu ophunzila bwino ndiodziwa ntchito yawo . Ndikukhulupilira kuti izi zakuthandizani.
Share your feedback