Mwana wanga, ichitu sichachilendo pamsikhu wakowo ayi. Apatu ndiye kuti thupi lako lasintha, wayamba kukula ndithu. Chilakolako cha anyamatachi ndi chifukwa chakuti watha nsinkhu.
Atsikana amnzako ansinkhu wakowu nawonso nkutheka akumvanso mmene ukumvera iwemu. Ena mwaiwo mwinanso nkutheka izi sakuzimvai. Pamenepo musadele nkhawa zimachitika ndithu ngakhale anyamata amazionanso.
Koma chenjezo ndilakuti izi sizitanthauza kuti upeze chibwenzi ayi. Kukhala ndi chibwenzi ndizonjoyetsa kwambiri komano tsoka lake ndilakuti zokhoma zimakhalaponso zambiri monga kubalansa pakati pasukulu ndi chibwenzi komanso kupeza nthawi yokhala ndi makolo ndi abale.
Kuwonjezera apo pamene uli paubwenzi nkhani yogonana imabwera. Langizo langa apa ndilakuti khalani tcheru komanso okonzeka pachilichonse chingabwele pamoyo wanu monga mimba zosayembekezela, matenda opatsilana pogonana. Konzekelani ndipo pasakhale ngati kuti munthu wina wake akukukakamizani zochita. Njira ina ndikuwonetsetsa mwapeza mzimayi yemwe mungamumasukile mumufotokozele akuthandizeni.
Share your feedback