Tayamba kuchotsera masiku ndipo Season 2 iyamba posachedwa. Nayi nyimbo yatsopano ndi vidiyo yake, Panga Zako, kuti itisangalatse pamene tikudikila ma episode atsopano a Zathu Pa Wailesi ma sabata akubwelawa.
Atamaliza photoshoot nkupanga Band yawo mu vidiyo ya Sitigonja; Xander, T-Reel, Mphatso, Chikondi, JP ndi Annetti anakhalanso nkupanga nyimbo ina yatsopano yosangalatsa . Akukumana ndi zopsinja zambili chifukwa Aunt ake a Chikondi amamukaniza Chikondi kukhala mu Band ya anyamata ndi atsikana. Koma ndi thandizo lochoka kwa Gogo Aunt Nelly anamulola Chikondi ndipo anakaimba limodzi ndi Band yonse. Zonsezi tizipeza mu Season2.
Mverani ndikupanga download Panga Zako
Pa Free Basics Mverani ndikupanga download
Mverani ndikupanga download Panga Zako Video:
MBC Radio 2 - Lolemba 15.30, Lachitatu 15.30, Loweluka 17.00
Zodiak - Lolemba 14:05, Lachisanu 15:30, Lamulungu 13:30
YONECO - Lachiwiri 16.30, Lachinayi 16.30, Loweluka 16.30
Voice of Livingstonia - Lachiwiri 16.30, Lachisanu 16.30, Loweluka 16.30
Share your feedback