Tikayelekeza ambiri ayife ndi inu chidwi chagona pakuti mudziwe makono kunjaku kwangwanji. Koma ngati muli pasukulu nkhawa ndiyakuti mayeso akayandikila kuphanda kumasowetsa Mtendere, sichoncho?
Komanso mukagwila buku mwanjomba mapeto ake zimadzakuthina. Nanji mukadumphitsa tsiku osamwela!?
Njira yabwino ndikupeza chinsinsi cha mmene mungamaphandile. Mukatelo mudzafewetsa moyo- kuphanda kwaphweka. Pezani nthawi yapadela ndi malo oyenela. Mwachitsanzo kukhitchini patebulo kapena kutandala ola limodzi kwamnzako mukaweluka kusukulu.
Apatu ndikosavuta kutsatila ndondomekoyi nanji malo ndi nthawi zapazeka- chatsala ndi kuzizoloweza basi.
Gawani ntchito zazing’ono pazokha. Siziyang’ana kuti kuphandako mukuchalira mayeso aboma kapena oyeselera ngakhale ntchito imene ikadza siyanitsani ndi zolinga zake. Ntchito yambiri imatangwanikitsa. Pamene mwathana ndi zolinga zazing’ono moyo umapepuka ngati watemela mangolomela.
Pumulani. Mkati kati mwakuphanda ngakhale mwamaphunziro ndibwino kupuma kaye. Mutha kudzithemba kuti ndinu kamuna koma ubongo umafunika kupumako. Pamphindi zokwana 45 kapena ola limene pumani mphindi khumi.
Yesani kusiya mabukuwo kaye. Pitani panja mupitidwe mphepo. Mutha kutchata pang’ono ndi mphwanu kapena kupanga ka tiyi. Komano osati monse mwapitila ndiomwewo ayi chipemba chimathawa.
Pezani njira yanu yophandila. Ena amawona kuti kukopa notsi ndinjira yabwino yophandila. Ena amaona ngati kuwelenga mofuula ndiye zilowa bwino. Ena amamva bwino akakhala pakati paamnzawo nkumakambilana. Ndibwino kukhala ndi nthawi ndikuyeselela njira zonsezi. Imene yagwirayo ndiyomweyo. Nthawi zina nkutheka kuti pali maphunziro oti akufunika njira yosiyana ndi maphunziro ena.
Zabwino zonse, apatu mwatolapo kanthu. Tiyeni nazo! Kumbukilani: Sizikudalira kukhala pasukulu pokha ayi koma pachilichonse mukuchita lingalirani kuti pali chinsinsi ndithu chomwe mungachite pamene mwapeza vuto kaya pamaphunziro. Tayesani.
Share your feedback