Kudzikhulupilira mwini wekha mkalasi ndichithu chamtengo wapatali. Nthawi zonse ndimanyumwa kuti ndiwawuze aphunzitsi abweleze pomwe sindinamvetse, ndimakanika. Olo kuti ndikweze dzanja ndiyankhe funso ndimalephela. Amnzanga amadabwa nane zoti ndine wanzeru ngati bodza.
Koma Anna mnzanga wapamtima ndie ndi nkhani ina. Amadzikhulupilira. Mwachidziwikile ndipeza magiredi abwino ndipo ndili ndi mpata wosankha chomwe ndikufuna pa moyo wanga. Zidzandithandiza kupititsa maphunziro anga patsogolo olo nditati ndipeze ntchito ndidzachita bwino
Anna ndiye kuchimake kwamalangizo. Pali chinsinsi chomwe anandibenthulirako kuti ndipambane sukulu. Inunso zingakukankheni.
• Chinsinsi choyamba. Funsani nthawi yomweyo pomwe simunamve musakhale chete kudikila kuti mufunse panthawi ina
• Chachiwiri. Ngati mwasautsidwa kulibwino kutsalira poweluka kuti mukumane ndi aphunzitsi pawiri akulongosololeni momveka bwino lomwe. Uzani mnzanu akupelekezeni musakhale nokha.
• Chachitatu. Musataye nthawi ndi anthu ena omwe ntchito yawo ndikukugwetsani mphwayi kaya kukusekani. Ikani mtima pamaphunziro basi. Zinazo musazilabadile.
Koma chinsinsi china chapadela chomwe Anna anandibenthulira nchakuti,” aliyense amawopa kumuweluzidwa ngakhale ine ndemwe. Kulimba mtima, pokweza dzanja mkalasi sikutanthauza kuti mantha ulibe ayi.”
Share your feedback