Zoyenela kukhala nazo
Ndondomeko yoyamba
Ndondomeko yoyamba ndikulondoloza mulingo wa Kansalu kapadi yako, tengani pepala lolimbilapo kuti mupange chifanizo chake cha padi. Jambulani mapiko ake 25cm mulitali ndi 17.5cm ngati mulingo woyenela wa chifanizo cha kansalu kapadi.
Ndi chifanizo chachiwirichi onetsetsani kuti mulitali mwatalikitsa ndithu kuti mapiko afanane chakumbuyo, kenako tsekani mabowo onse. Gwiritsani ntchito isezi kuti chifanizo chilingane bwino ndi chojambulidwa chija.
Ndondomeko yachiwiri
Dulani nsalu yokhuthala pakati kupanga magawo awiri 30 ndi 30cm iliyonse. Gwiritsani ntchito chifanizo chija poyika pamodzi ndi tinsalu tiwiri tija tokhuthala kuphatikizanso nsalu ya sumbulera pamwamba pa chifanizo china chija ndipo gwiritsani ntchito choko kapena pensulo, mkala pojambula motsatila chifanizo chija.
padika, ndi kupanga mapiko. Mapikowa akule ndithu kuti athe kukumana pansi pa chovala chamkati chanu.
Uku ndi kunja kwa padi. Tiyitcha kuti kansaza kachiwiri ngati B, ndie tilinso ndi kansaza koyamba A ndi Flannel C yomwe ndi nsalu ya sumbulera.
Ndondomeko yachitatu
Dulani pawiri kasanza kachiwiri B ndi kamodzi kansaza koyamba A ndi C ya padi iliyonse.
Ndondomeko yachinayi
Ikani mbali zofanana zonse pamodzi (tembenuzani mkati). Sokani magawo awiri onse a kansaza B pamodzi, siyani mpata wa 3cm kuti mutembenuze kunja kwake kachiwiri.
Mukuyenela kugwiritsa ntchito isezi kuti muthe kupanga tomangila mmbalimmbali, kuti pamene mukutembenuza kathe kukhala mosapindika. Sitani ngati muli ndi simbi.
Ndondomeko yachisanu
Sokani mpata unasiyidwa ndikuutseka bwino ndi dzanja.
Mukatha kusoka, sitani. Kenako, sitani mapiko kuti alumikizane ngati momwe zikuwonekela pa chinthunzipa.
Share your feedback