Ndikovuta kudziwa kuti mmene ndagonana ndi uyu mosadziteteza ndatenga kapena sindinatenge mimba. Koma dziwani kuti ngati mwagonana mosadziteteza ndichapafupi kutenga mimba chifukwa chakuti ndichapafupi kuti umuna utakase dzila lamayi.
Ngati mukufuna kupewa mimba kuli bwino kudziletsa kapena kugwiritsa ntchito condom.Komanso mutha kupita kuchiptala kukamva njira zina zopewela mimba ngati mwagonana mosaziteteza. Koma kuti mudziwe ngati mwatenga mimba pogonana mutha kudziwa pamene mwaphonya kupita kumwezi. Mukaona kuti izi zili chonchi ndibwino kupita kuchipatala akakuyezeni mimba.
Share your feedback