• English
  • Menu

Kagwiritsidwe ntchito kake

Pofuna kuwerenga tsamba la www.zathu.mw painternet mukuyenela kutsata njira yokhayo yoyenela. Tikanyalanyaza ndiye kuti taswa lamulo. Mudzalandila chenjezo kuti mwasempha lamulo ndipo nthawi yomweyo simudzaloledwanso patsambali.

Malamulo ndi awa: nkhanza komanso kutonzana sikuloledwa patsambali. Lemekezani achichepele ndipo pewani kutukwana, mwano ngakhale kutumiza matsamba ena apa internet olawula kwa amnzanu. Pewani kupeleka mbiri ya moyo wanu makamaka bisani dzina lanu lenileni (gwiritsani dzina lantchedzelo lanu ‘username’), bisani zaka zanu, keyala yanu ngakhale yapainternet, sukulu, nambala ya foni, musawululenso dzina lamakolo anu ndi omwe amakusungani, ndipo samalani nambala yanu ya chinsinsi.

Pewani kupanga mgwirizano ndi anthu omwe mwakumana nawo kumene patsambali. Ngati nkotheka kuti mwalumikizana chonde kakumaneni nawo pamene muli ndi munthu pambalipa osati nokha.

Ngati zaka zanu ndizochepela 13, onetsetsani kuti mwalowa patsambali potsatila chilolezo chamakolo kapena munthu wamkulu akuyang'anileni.

Tsamba la Zathu.com ndilokomela aliyense makamaka wazaka zosachepela 13.

  • Facebook Zathu Pa Wailesi
  • Home
  • Nkhani Zathu
  • Show Yathu
  • Nyimbo Zathu
  • Moyo Wathu
  • Za Zathu
  • Kagwiritsidwe ntchito kake
  • Keyala
  • Ndondomeko ya Malamulo

© 2025 Zathu. All Rights Reserved.