Mawu otsogolera: Malamulo otsatilawa akufotokoza mmene tingatetezele, kusonkhanitsa ndi kugwiritsa ntchito uthenga uliwonse mwatitumizila pamene mukugwiritsa zinthu za Zathu. Dziwani ndichapafupi kulipilitsidwa.
Zathu ndi chikonzero cha Girl Effect, bungwe lachifundo, lovomelezeka ndi Boma la England komanso Wales. Bungweli lili mukalembela wa makampani. Nambala ya kampani ya Bungweli ndi 07516619 komanso nambala ya bungwe lachifundoli ndi 1141155.
Umwini wonse ngakhale kayendetsedwe ka Zathu kali mmanja mwa Girl Effect . Zathu ili ndi nthambi zingapo monga; tsamba lapainternet la Zathu.com ndi matsamba ena, tsamba la Facebook, Zathu Pawayilesi mu sabata iliyonse, uthenga wa pafoni, zochitika (ngati mashow), makilabu komanso buku la magazine.
Cholinga cha Zathu ndikupeleka uthenga wofunika komanso chisangalalo kwa atsikana ndi anyamata.
Sizachibwana kusunga Chinsinsi. Tadzipeleka mwathunthu poteteza ndi kusamala chinsinsi cha mbiri ya moyo wanu. Ndondomekoyi ikufotokoza mmene tisonkhanitsile ndi kugwiritsa ntchito uthenga/ mbiri ya moyo wanu yomwe mwatipatsa.
Ngati muli ndi funso lina lililonse lembani kalata yapa internet ndi kutumiza ku keyala ya tsamba lathu ya internet iyi hello@zathu.mw
Pamene mwagwiritsa ntchito Zathu ndiye kuti mwagawilanso ife mbiri yamoyo wanu munjira izi; Kulembetsa kapena kulipila umembala wanu pa Zathu, kutenga nawo mbali pa zisankho kapena pa kafukufuku; Kugawana uthenga (mwachitsanzo kupeleka ndemanga kapena kutumiza zithunzi) kupsolera ku mbali zonse za Zathu komanso uthenga uli wonse umene mwapata pogwiritsa ntchito Zathu.
Pamene mukugwiritsa ntchito Zathu ife tidzatolera mbiri yamoyo wanu yokhudza izi; dzina lanu, chaka chobadwila, umunthu wanu ngati muli mwamuna kapena mtsikana, nambala yanu ya foni ndi keyala yanu yapainternet. Kuphatikizanso uthenga uli wonse talandila kuchokela mnthawi imene mukutenga mbali pa zisankho kapena kafukufuku olo uthenga wanu wina wapang’ono pokha maka pamene mukugwiritsa ntchito Zathu (potengela kuti mwalowa kangati pa tsamba lathu)
Tigwiritsa ntchito mbili yamoyo wanu mumnjira zambiri; kulongosola umembala kapena malipilidwe a umembala wanu, kupititsila mtsogolo Zathu ndi ntchito zake, pakafukufuku komanso malipoti ammene tikugwilira ntchito.
Mbiri ya moyo wanu idzasamalidwa kapena kugawidwa kwa wena motsatana ndi lamulo lililonse limene lingatipemphe kutelo.
Titha kugawana ndi wena pokhapokha ngati tikuwathandiza pankhani yakafukufuku koma tidzawonetsetsa kuti asakuzindikileni kuti inu ndindani.
Pofuna Kuteteza mbiri yanu timagwiritsa zinthu zingapo. Mbiri yanu yasungidwa mmalo wotetezedwa kwambiri amene amayang’anilidwa ndi anthu wosankhidwa angapo.
Komabe ngakhale zili choncho sitinganene motsindika kuti uthenga uliwonse wotumizidwa pa internet uli wotetezedwa mokwanila ayi. Izi zikutanthauza kuti ngakhale tingayesetse kuteteza mbiri yanu imene mwatipatsa tilibe chitsimikizo chenicheni za chitetezo chake painternet. Mvetsetsani kunena kuti mwatipatsa mbiri yanu mwakufuna kwanu.
Pamene mwatipatsa ife mbiri ya moyo ndi chinsinsi chanu ndiye kuti mwativomela kusonkhanitsa ndi kugwiritsa ntchito mbiri yanuyo chomwechonso ife titsata malamulo onse amene ali mundondomeko yathuyi.
Timagwira ntchito padziko lonse lapansi choncho uthenga wina umatumizidwa ku Mayiko ena. Apatu ndiye kuti inu mwatilola ife kugawana mbiri yanu ndi mayiko ena osati Malawi yokha ayi, ngati nkofunika kutero koma motsata ndondomekoyi.
Mayiko enawa sangateteze uthengawu/ mbiri yanu mmene lingatetezele dziko la Malawi koma ngati pangakhale kupelekedwa kuli konse kwa mbiri yanu ndie kuti tidzakhazikitsa mgwirizano pakati pathu kuti mbiri yanu itetezedwe.
Ngati mwafuna kulanda chilolezo chanu lembelani kalata ya painterneti ku keyala iyi; hello@zathu.mw
Chilichonse chokhudza mulingo wa nthawi imene tingatenge posunga mbiri yamoyo wanu zitengela chilolezo chanu chimene mwatipatsa. Komanso pena zitha kutengela kuti ifeyo tasangalatsidwa bwanji ndi mbiri yanu mpaka kulowa nayo mukawundula wathu. Chisamaliro chake chikukhudza kayendetsedwe ka umembala ndi malipilidwe ake komanso mbili yanu imene.
Tisunga mbiri ya moyo wanu kutengela ndikuti inunso mukugwiritsabe ntchito Zathu. Ngati mwalanda chilolezo ifenso tifafaniza mbiri yanu mukawundula wathu. Chimene tingasunge ndi uthenga wina umene munawupeleka posadzitchula dzina.
Muli ndi ufulu wopeza uthenga/ mbiri yanu ina iliyonse imene ife tikusunga. Komanso muli ndi ufulu wotipempha kukonza mbiri yanu ngati penapake panalakwika kapena kutiwuza tifafanize pena paliponse.
Ndiufulu wanu kulumikizana nafe pogwiritsa ntchito keyala ya internet yanenedwa mu ndondomekomu koyambilira kuja.
Ngati mwakhumudwa ndi momwe tagwiritsila mbiri yanu mukuyenela kupeleka dandaulo.
Ngati mbiri ya moyo wanu yasintha tiwuzeni kuti tithe kusintha nthawi yomweyo polumikizana nafe kupsolera pa keyala ya internet yathuyo. Ife titha kusintha ndondomekoyi kutengelanso kusintha kwa malamulo adziko.
1. Tanthauzo la Macookie komanso zida zosakatulira internet
Macookie ndi fayelo yosungila timauthenga totsitsidwa mu komputa yanu kapena pafoni kuchokela patsamba lainternet. Matsamba ainternet ambiri amagwiritsa ntchito macookie. MaCookie amathandiza inu kusakatula ndi kuwerenga matsamba ena komanso kukuzindikilani inu ngati munthu yemwe muli patsambalo. Macookie amathandizanso inu kuti muthe kulowa paliponse patsamba lathu la internet.
Mndandanda wa maCookie ukupezeka pa mndandanda wa maCookie patsamba lathu.
2. Kugwiritsa ntchito komanso kufafaniza maCookie
Pamene mwalowa pa Zathu.com mulandila chidziwitso kuti timagwiritsa ntchito maCookie. MaCookie ayikidwa poyambilira kuti tiwonetse mwadongosolo tsamba la Zathu.
Mukapitiliza kulowa patsamba la Zathu maCookie ambiri adzawoneka pa komputa komanso foni yanu. Ngati simukufuna kulandila maCookie mutha kutelo mumnjira izi;
Dinani njira yotsekulira internet / browser ndipo mudzasankha kuti ikanize maCookie onse kupatula matsamba okhawo mukuwakhulupilira kapena vomelani maCookie ochokela kumatsamba amene mukulowapo.
Kumbukilani kuti ngati maCookie aletsedwa ndiye kuti Zathu mwasemphana nayo. Kuti mumve zambiri lowani pa tsamba la allaboutcookies.org
3. Mitundu yathu ya maCookie
Mitundu ya maCookie ili motere; maCookie ofunika kwambiri mwakuti simungachitilenso mwina. MaCookie ndiwothandiza kuti muthe kulowa malo aliwonse apatsamba ngakhale malo ena obisika.
MaCookie amatolera uthenga umene umakuwonetsani mmene mungagwiritsile ntchito tsamba lathu, matsamba amene mumalowa nthawi zambiri komanso ngati mwapeza vuto pamatsambawa. Timagwiritsa ntchito maCookie pa tsamba lathu kuti litukuke ndi kuwoneka bwino.
MaCookie amathandiza kuti tizitha kukumbuka zosankha zathu monga dzina la keyala yanu pa kalata ya internet komanso kuti matsamba awoneke bwino.