English Chichewa
Menu Sign up Search
Our Lives
f

CHITETEZO CHA MAUTHENGA ANU

Uthenga wa padela kwa ma fans athu......

Read more

Monga mukudziwa kuti timakonda kucheza ndi Omvera athu kudzela mma uthenga apafoni, tsamba la intaneti ya zathu.mw ndi pa facebook page ya Zathu .

Komano, pakatipa tazindikila kuti kuyambila pa 22nd August kufika pa 27th October 2018 mauthenga omwe amatumizidwa ku nambala yathu yoyambila 0888353535 samalandilidwa kuno ku Zathu.

Izi zikutanthauza kuti ngati munayesela kuimba kapena kutumiza uthenga ku nambala ya 0888 munthawi imeneyi uthenga wanu ndi nambala ya foni yanu zinafikila munthu wina.

Ngati munthu wina wake analumikizana nanu poyankha uthenga womwe munamutumizila kuyambila pa 22nd August kufikila pa 27th October, 2018 sitinali ife a Zathu ndipo mukuyenela kutidziwitsa potimuza uthenga ku hello@zathu.mw

Back to Top