Uli ndi ufulu wamaphunzilo

Anyamata ndi atsikana padzikolonse akuzindikila kuti maphunzilo ndiye tsogolo

Mnyamata aliyense ngakhale mtsikana amene ali ndi ufulu wamaphunziro ndipo akuyenera kukhala pasukulu yapafupi ndikwawo popanda kuwopsezedwa. Musathawire sukulu pawindo ndi tsogolo lanu.

Akuluakulu ena angapo ananenapo mwachindunji mawu achilimbikitso kuti:

“Chilimikani ngati mukufa mawa. Phunzilani mozama ngati mukhala mpaka muyaya.” – Mahatma Gandhi, mtsogoleri wa Indian independence movement

“Maphunziro ndichida chokhacho chomwe chingasinthe dziko” – Mtsogoleri wakale wa dziko la South African yemwenso ndi Nobel Peace Prize winner Nelson Mandela

“Tikaphunzitsa atsikana dzikonso limatukuka.” – Mkazi wa mtsogoleri wa America, Michelle Obama

“Ife ndife wosinthika momwe tifunila. Kusintha sikudalira wina adze asinthe zinthu kapena nyengo iliyonse ayi.” – Bipasha Basu, Mkozi wa mafilimu ku India

“Pamene ufulu wawina ndi mnzake ufanana ndipo pali kulingana kwa mwayi wawina aliyense mabanja athu, madela ndi mayiko adzapita patsogolo.” – Dr Babatunde Osotimehin, Nigerian public health expert and executive at the United Nations

“Ndimakhulupirila kuti ukaphunzitsa mtsikana ndie kuti wamanga mudzi.” – Mfumukazi waku Rania kuJordan

Share your feedback