Chikuchitika ndichani nthupi mwanga?

Chisodzela … aliyense anadutsamo!

Mwina mwazindikila kuti thupi lanu lasintha, mwayamba kukula. Ichi ndie chilengedwe kapena kuti nthawi yachisodzela. Siiwenso mtsikana koma mzimayi ndipo mnyamata ndiwe nzibambo tsopano.

Chisodzela? Ndichani?

Wina aliyense ndiosiyana ndi mnzake koma chimene tifanana tonse pakati paanyamata ndi atsikana ndipoti tonse timadutsa muuchisodzela.

Apa ndie kuti munthu akukula kukhwima nzeru. Uchisodzela umayamba zaka 7 olo 8 ndipo pamapita zaka zinayi olo zisanu. Zakazi zilibe kanthu kwenikweni chachikulu ndichakuti tonse timadutsa munthawiyi.

Malire

Pamene thupi layamba kusintha pali zambiri muyenela kudziwa

  • Umatalika (Tholo)
  • Thupi limanona
  • Ziphuphu kumaso
  • Atsikana amabwera mahip , anyamata mapewa kukula
  • Tsitis kukhwapa komanso kumaliseche
  • Anyamata kumela ndevu, tsitsi pamtima ndi mmiyendo, mmanja komanso kumaliseche
  • Atsikana amapita kumwezi ndi kumera mawere
  • Anyamata amadzikodzela ndipo maliseche awo amakula. Komanso amayamba Besi.

Kumwezi

Pamene mtsikana watha msinkhu ndiye kuti ndi nthawi yachisodzela ndipo amataya magazi kwamasiku atatu olo asanu.

Mtsikana amakhala kumwezi kamodzi pamwezi pamenepa thupi limakhala lilitcheru nthawi isanafike. Pamene mtsikana ali kumwezi ndie kuti nkosavuta kutenga mimba kenako kubadwitsa mwana.

Kudzikodzela mwa anyamata

Anyamata nawonso akakhwima nthupi mumayamba kutentha. Ngakhale kutulo kumene amataya ukala. Nthawi zina madzidzimuka pena angogoneleza osadziwa kanthu. Nthawiyi imakhala yosawutsa komanso pena yonyaditsa koma chachikulu nchakuti aliyense amadutsa munthawiyi.

Share your feedback