Muumodzi wathu muli mphamvu

Tikagwila ntchito limodzi kusintha kulipo

Muumodzi wathu tingaike dziko patali

Kuti zitheke tichite izi:

Pezani anthu akunga iwe

Pezani anthu achinyamata amnzanu amene zochita zawo ndizanu ndizimodzi kaya mukawapezela pasukulu, mmudzi bolani mukuchita zimodzi. Gwirizanani nthawi yokumanilana. Kwa amene amakonda nyimbo awunikenso ngati pali ena amnzawo okondanso nyimbo ndipo ndibwino kuyamba marehearsal mukaweluka kusukulu.

Zikachuluka sizidyeka

Khalani ndi ndondomeko yazolinga zanu yomveka bwino. Mukufunanji? Osanyentchera kuti simunayambe ndi moto. Zikachuuka sizidyeka. Mwina mumdela lanu pali anyamata ndi atsikana ena amavutika kupita kusukulu ndipo inu mukuwona kuti mpata ndiomwewu muwagwile dzanja azitha kuyenda bwino.

Mveranani

Sitonse timaganiza mofananaa. Chanzeru pagulu kuti ziyende ndikumverana wina ndi mnzake komanso kulemekeza zonena amnzako.

Dalilanani

Pangavute chotani osatayana. Mangani ubale wina ndi mnzake kaya ndi wam’banja, aziphunzitsi tonse tigwirane manja

Phunzitsanani

Kudzela kumaluso athu tiyeni tithandizane.Ngati ndiwe dolo wamasamu amnzako apezelepo mwayi paiwe. Chimodzimodzinso telala atha kumusokela mnzake waluso lina chovala ngati tonse tithandizana.

Osagwetsana mphwayi

Ukakhala pakati paanthu ozolowela zamijedu palibe chomwe ungaphulepo. Usagwe mphwayi ndizonena zaanthu oterewa peza amnzako olimbikitsana nawo.

Atsikana ndi anyamata osangokhalira manyado koma mukakhala limodzi gawanani nzeru ndi maluso kuti moyo wanu upite mtsogolo.

Share your feedback