Ndili ndi business ndipo ikuyenda bwino kwambiri. Kodi ndibwino kusiya sukulu ndikuyika chidwi changa pabusiness?

Okondeka bwanawe, ndichosangalatsa kupeza mwayi wolankhulana ndi anthu ngati inu amene business yanu ikuyenda. Langizo langa nali. Pitiliza sukulu. Maphunziro ndiwofunika kwambili. Maphunzilo ndi njira yokhayo imene ingakweze business yako patsogolo komanso kupeza phindu lambiri. Apatu business ikukula muthanso kulemba anthu osowa ntchito.

Mwachidule, pitilizani sukulu kwinaku mukuchita business. Ngati mwapata mwayi wopitiliza maphunzilo mpakana ku koleji ndietu ukachenjede wake ukagwilizane ndi za business yako.

Ndichimodzimodzi anthu ena ali ndi luso loyimba ena lazamasewera choncho ngati ungakwanitse sukulu komanso luso nthawi yomweyo apo ndie kuti wapha mbalame ziwiri ndi mwala umodzi.

Share your feedback