Dzina langa ndi Moses. Ndine namwino. Ndimagwila ntchito mzipatala zaBoma.
Pachiyambi penipeni ndinalibe Khumbo lokhala namwino. Nditalemba mayeso olowela ku University, entrance exams a University of Malawi anandisiya.
Patapita kanthawi ndinaona munyuzi a Malawi College of Health Sciences akulembetsa mayina a sukulu. Mwayi wanga unali womwewu wopititsa maphunzilo anga patsogolo komanso kuyamba ntchito, career yamtundu wina kusiyana ndi zokhumba zanga m'mbuyomu.
Ndinapanga apply ku pulogalamu ya unamwinoyi nthawi yomweyo ndikutengedwa. Makolo ndi amnzanga ena anandiwuza kuti sindinapange chisankho chabwino. Amkati unamwino ndi ntchito ya atsikana osati mnyamata.
Nditangoyamba maphunzilo ndinaona kuti unamwino ndi pulogaramu yabwino kwambiri kuposa momwe ndinkaganizila poyamba.
Pano palibenso wina angaletse kuti unamwinonso ndi ntchito ya amuna ngakhale ambiri mwaife timaganizabe kuti amuna sakuyenela kukhala anamwino. Ukutu kumangokhala kuganiza mopelewera basi.
Amuna ngakhalenso akazi atha kukhala anamwino abwino chitsanzo chake ndi ineyo. Palibe ntchito yomwe tinganeneletu kuti ndiya amuna kapena akazi ayi. Ndikotheka kukhala kapena kuchita chinthu ngati uli ndi masomphenya. Palibe china chilichonse choletsa.
Share your feedback