Okondeka agogo anthu ena amati njira zakulera ndizaamayi osati atsikanafe. Kodi ineyo ngati mtsikana nditha kuyamba njira zakulera?

Zikomo kwambili Alice chifukwa chafunso lako. Nkhani yakulera kwambiri yatsamila poti timvetsetse uthenga kenako tithe kupanga chiganizo chakuti tiyambe banja kapena kudziteteza pogonana. Tikakamba za njira zakulera ndie kuti tikukambanso za kubadwitsa mwana, kutenga mimba panthawi yoyenelera komanso kupewa kutenga mimba ngati usanakonzeke.

Kulera ndi ufulu wawina aliyense kaya ndi nzimayi ngakhale mtsikana amene. Umu ndimomwe mabungwe ena owona maufulu atsikana amanenela. Atsikana akatha nsinkhu ziwalo zawo zimakhala ndikuthekela kobeleka. Izi zikutanthauza kuti ngati sakulera atha kutenga mimba yosakonzekela mosavuta. Ndikuwona ngati ndichanzeru atsikana kusankha njira yakulera yomwe akuiwona bwino. Koma athanso kudziletsa. Atha kugwiritsa ntchito ma condom pogonana komanso kupita kuchipatala kukatenga upangili wabwino wa zakulera kuti apewe mimba zosayembekezela kapena matenda opatsilana pogonana monga mankhwala oteteza mimba yapangozi. Ngati wachipatala akupatsa mankhwalawa pomweponso akuwuza kagwiritsidwe ntchito kake. Koma munthu woyenela kukupatsa uphungu wabwino pazakulera ndi Dokotala basi

Share your feedback