Okondeka Gogo, ndingadziwe bwanji kuti munthu uyu (mtsikana/ mnyamata) ndi woyenera kukhala mnzanga?

Okondeka Jeffery, munthu ameneyu akhale munthu amene umamasukilana naye komanso muli ndi zokonda zofanana.

Mwachitsanzo Ngati nonse mumakonda kuimba muthanso kumanga chimzake kupsolera pa kuimba. Monga mmene alili anthu amu sewero la Zathu omwe anapanga ubale chifukwa chakuimba. Pamene anakhala pachimzake ndi pomwe anadziwana kwambiri ndikuyamba kuthandizana komanso kusangalarila limodzi. Ichi ndi chitsanzo chimodzi chokha koma zokonda zanu zitha kukhala zina bola mukusangalala nazo.

Ngati mukuthandizana wina ndi mnzake, komanso kugwirizana ndi kulemekezana ndiye nchachidziwikile kuti munthu wina akhozanso kukhala mnzako. Kumbukilani kuti sizingayende ndendende mmene ndanenela koma izi ndi zinthu zina zoti muziyembekezele pamene mukuyamba chimzakendi munthu wina.

Share your feedback