Okondeka Gogo, kodi ndingalankhule bwanji ndi makolo anga zokhudza ziganizo zomwe angandipangile pa moyo wanga mopanda kuwakhumudwitsa?

Ndi chilimbikitso chapadela kuti waonetsa chidwi chofuna kumasukilana ndi makolo ako ...

Zikomo kwambiri chifukwa cha funsoli. Ndi chilimbikitso chapadela kuti waonetsa chidwi chofuna kumasukilana ndi makolo ako pa nkhani zokhudza moyo wako. Ganizo langa ndilakuti uyankhule nawo modekha.

Ukhale wodzikhulupilira komanso uwonetse kuti ukudziwa chomwe ukufuna ndipo wamanga nfundo. Mwachitsanzo, ngati makolo ako akufuna kuti uphunzire sukulu yoyendera koma iwe ukufuna yogonela pomwepo, awonetse ubwino wake wokhala pa sukulu yogonela pompo.

Njira ina, ndibwino kupeleka mpata kuti umve maganizo awo. Ukatelo zionetsakuti umalemekeza zonena zawo. Ndikukhulupilira kuti iweyo ndi makolo ako mumvetsesana ndikupeza njira yothandiza.

Share your feedback